BAMBO WINA WATEMEDWA MODETSA NKHAWA NDI MKAZ WAKE ATAMUPEZA AKUPANGA ZADAMA NDI MKAZI WINA



Bambo wina watemedwa pakhosi ndi mkazi wake ku Chigwiri m'boma la Lilongwe atamupeza akupanga zadama ndi mkazi wachibwezi. Izi zachitika potengera kuti mamunai wakhala akuzembera mkazi wake mwakanthawi zomwe zidapangitsa kuti mkaziyu ayambe kufufuza kumene kumapta mamunai. Mkaziyu adauzidwapo zakhalidwe komaso mayende mmene akuchitira mamunai zimene zidapangitsa kuti ayambe kafukufuku choncho mkaziyu adatenga pwitika ndikuyamba kulondola kumene kudali mamunai. Mkaziyu adawapezadi ndipo posakhalitsa adakhapa khosi lamamunai mopitilira zimene zidapangitsa kuti mamunai ataye magazi ochuluka kwambiri.

Zitachitika izi, mamunai adatengeredwa kuchipatala cha Kamuzu Central ku Lilongwe kumene adakalandila thandizo lamagazi komaso kusokedwa bala . Nkhanza mmabanja zilimo ndipo zikuchitika, zimaoneka zophweka mamuna akachitilidwa nkhanza , inde mkazi amatengeredwa kuchitokosi kapena kuti (police) pachingerezi koma chilango chake chimakhala chosiyana powakondera azimai pamene mamuna kuchita chimodzimodzi amakatsekeredwa kuchitokosi kumene amakagwira ntchito yakalavula gaga.



Timava kuti pasakhale kusiyana pakati pa amuna komaso akazi ndipo boma lidakhazikitsa lamulo la 50-50 campaign kutanthauza kuti tikhoza kugwira ntchito zofanana posatengera kuti uyu ndimkazi kapena kuti uyu ndimamuna. Mkazi akhoza kugwira ntchito zimene mamuna angathe kugwira koma tikapita pa nkhani ya nkhanza mmabanjamu timaona zilango zosiyana zikuperekedwa chosecho pali lamulo lakuti pasakhale kusiyana pakati mamuna komaso mkazi. Ndeno mafuso mkumati,, kodi ndende ( chitokosi kapena kuti police) zidamangidwira amuna okhaokha??, inde mamuna atapezeka kuti ndiye olakwa komano mkazi wakhetsa mwazi, ndipoyenera kuti mkaziyu asamangidwe??, nanga kodi ufulu okhala ndi moyo ulipo, ndipo ukutetezedwa ??. Awa ndi ena mwa mafuso amene amafusidwa potsatira zilango zimene zimaperekedwa.

Boma limaonetsetsa kuika njira kuti pasakhale kusiyana pakati pa amuna komaso akazi. Bambo wina adatsekeledwa mchitokosi atamenya mkazi wake. Ngakhale adali olakwa ndi mkaziyu komabe dandaulo lake silidaveke. Boma likuyenera kukhazikitsaso ndondomeko zina zokhwima zoyenera pothana ndi nkhanza mmabanja.

Kuonjezera apo , ndibwino kumakhutitsidwa ndiwachikondi amene mulinaye chifukwa mavuto ena timachita kuwayamba dala mwachitsazo bambo otemedwawa akadakhala okhutitsidwa ndi mkazi wawoi sadakatemedwa chonchi koma kamoyo ka uhule ndikamene kamativulalitsa, tikuyenera kuchepetsa chifukwa zotsatira zake tikutengelana matenda chifukwa chosadzigwira komaso tikuyenera kumasukirana kupatsana zimene wina akufuna chifukwa ngati tikulephera kumasukirana m'banja ndizimene wina amakasaka kwina kumene angakazipeze zimene amafunazo. Tikuyenera kumavetsetsana mmabanjamo chitukuko chiyambire mmenemo kenako chizionekera kudera kufikira dziko lose.

Mafumu komaso dziko latopa ndi nkhani zokulirana mitima. Mabanja ambiri amasokonezeka kamba ka nkhani zachuma. Mabanja ena amayambana akapeza chuma pamene nthawi imene anali amphawi amakondana kumapatsana ulemu, kutsazira nyimbo yakatswiri Skeffa Chimoto. Azibambo ena amayamba moyo umenewu atapeza ndalama choncho mkazi wawo sawoneka ngati munthu koma amafuna kuti apeze mkazi wina woti oti adye naye ndalama zimene atulutsa ndi mkazi wawo wapanyumba. Funso mkumati, mkazi wapanyumbai kuti wazindikira mayendedwe achilendo amene mamunai wayamba pomafika pokadya ndalama zimene apezera limodzi ndi mkaziyu atamupeza akupanga zachikondi ndi mkazi wina zingathe bwanji??, tikuyenera kusamala kwambiri maka nyengo yokolora ino. Inuso akazi odikira ndalama zogwira ntchito mkazi mzanu mudzalandira mabala chifukwa chakhalidwe lanu ndizimene mkazi amakhala onyasidwa ndimakhalidwe amamuna wakeyo choncho amatha kupanga chilichose fofuna kuteteza katundu komaso udindo wamamuna wakeyo pankhani zachitukuko.

Taonapo imfa zambiri zobwera chifukwa choswerana mitima mmabanja. Izi zimachitika pamene mamuna wasiya mkazi wake amene wapanga naye chitukuko mkudzakwatira mkazi wina. Zimachika nthawi ina kuti anthuwa amadzabwererana banja likatha koma mapeto ake amatengerana matenda ngati anayamba chitukuko chimathera pompo chifukwa cha uhule.



Tikuyenera kukhala anthu olimbikira ntchito kusi chitukuko chipite patsogolo komaso kukhala odalilana pabanja komaso dziko chifukwa mu umodzi muli mphamvu. Tiyeni tithetse nkhanza, titukule Malawi kuti likhale dziko lokomera aliyese.

Reported by Shombe Gaven

Journalist 👏

Comments

Post a Comment

Popular posts from this blog

UNICEF LAUNCHES US$ 20 MILLION APPEAL TO SUPPORT 96,000 CHILDREN AFFECTED BY RECENT EARTHQUAKE IN WESTERN AFGHANISTAN

WHO GLOBAL MALARIA PROGRAMME LAUNCHES NEW OPERATION STRATEGY